Nehemiah 7

1Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

4Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

6Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
7
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

 8Zidzukulu za Parosi 2,172
 9Zidzukulu za Sefatiya 372
 10Zidzukulu za Ara 652
 11Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,818
 12Zidzukulu za Elamu 1,254
 13Zidzukulu za Zatu 845
 14Zidzukulu za Zakai 760
 15Zidzukulu za Binuyi 648
 16Zidzukulu za Bebai 628
 17Zidzukulu za Azigadi 2,322
 18Zidzukulu za Adonikamu 667
 19Zidzukulu za Abigivai 2,067
 20Zidzukulu za Adini 655
 21Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98
 22Zidzukulu za Hasumu 328
 23Zidzukulu za Bezayi 324
 24Zidzukulu za Harifu 112
 25Zidzukulu za Gibiyoni 95.

25
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.

 26Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa 188
 27Anthu a ku Anatoti 128
 28Anthu a ku Beti-Azimaveti 42
 29Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 743
 30Anthu a ku Rama ndi Geba 621
 31Anthu a ku Mikimasi 122
 32Anthu a ku Beteli ndi Ai 123
 33Anthu a ku Nebo winayo 52
 34Ana a Elamu wina 1,254
 35Zidzukulu za Harimu 320
 36Zidzukulu za Yeriko 345
 37Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono 721
 38Zidzukulu za Senaya 3,930.


39
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 973
 40Zidzukulu za Imeri 1,052
 41Zidzukulu za Pasi-Huri 1,247
 42Zidzukulu za Harimu 1,017.


43Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya     74.


44Anthu oyimba:

   Zidzukulu za Asafu     148.


45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
   Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai     138.


46
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
 47Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
 48Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
 49Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
 50Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
 51Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
 52Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
 53Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
 54Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
 55Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
 56Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.


57
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za
   Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
 58zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
 59zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu
   zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
 60Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392.


61
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
 62Zidzukulu za
   Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642.


63Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za
Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
64Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
73Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Copyright information for NyaCCL